Skip to main content

Getting started with DHIS2 via Lenovo Tab 10

Lenovo Tab 10, imalowa simcard koma imakanika kulandila ma calls komanso imakanika kuyimbila anthu ena. Pa chifukwa ichi kulowetsa ma units kumavutilapo, koma ma SMS amafika bwino bwino. (Pangani phone yanu isamadye maunits kwambiri)

Phone imeneyi imadalila WiFi Access point, kapena kutumizilidwa ma units, komaso internet data kuchoka pa phone ina (kuti mudziwe zambiri zokhudza WiFi)

Njira yachidule yolowetsa ma units pa phone imeneyi kudzela TNM

Ngati muli ndi simcard ya TNM, Pitani ku tsamba ili topup.tnm.co.mw/prepaid/ ndipo ndiyaulele. Choyamba mukafika pa tsamba limeneli imaonetselatu phone number yanu, balance ya ma units, current bundle status, etc.

Mukaonetsetsa m'mwambamo pali "recharge". Mukapita pamenepo mupeza polemba number yanu, m'munsi mwake muli poyenela kulowetsa ma numbers omwe ali pa scratch card yanu. Kenako pansi pake pali button la green lomwe mumasindikiza mukamaliza kulowetsa ma numbers apa scratch card, ndipo ngati network ili bwino sizichedwaso pompo SMS yodziwitsa kuti ma units alowa imabwela.

Ena atha kufuna kupanga recharge number ina kudzelaso njira yomweyi posankha kabokosi kakang'ono pamwambapo komwe kamaloleza kusintha phone number yomwe kupite ma units.

Mukatha kulowetsa ma units, mutha kugulanso internet bundle posankha mawu olembedwa "bundle" pambali pa "recharge" kenako mutha kusankha bundle yaku mtima kwanu.

Getting started with DHIS2 after airtime top up

Pa phone yanu tsekulani Google chrome, pitani Ku tsamba ili; dhis2.health.gov.mw

Choyamba mukafika pa tsamba limeneli mumafikila kumene mukupemphedwa kuti mupange log in kugwiritsa ntchito credentials provided by your HMISo.
Koma musadalowetse ma credentials onetsetsani ma settings a google chrome mwasankha pa "desktop site"

Mukasintha ma settings amenewo, nokha muzindikila kusintha pa tsambalo chifukwa pabwela mbendela ya dziko la Malawi.

Alright moving on, after entering the right credentials mumafikila pa tsamba lotchedwa "Dashboard" pa tsamba limeneli pamapezeka zinthu zosiyanasiyana. Kufika pamenepa ndikhulupilila mwakwanitsa kugwilitsa ntchito Lenovo tab 10 kuti mufike pa dhis2. Kwa omwe angafune kulowetsa ma Report kapena zina zotelo tsatilani zithunzi mmunsimu.


mukasankha pamenepo ikuonetsani mbali zomwe zomwe mungapite.

Thank you, for reading along patiently. For further illustration, masukani ndikupempha mbali yomwe mungafune kudziwitsitsa.

Comments